CHINDOKO NDI CHLAMYDIA (GONORRHEA NDI CHLAMYDIA)
- Nthenda ya chindoko imayamba pokha pokha ngati
mkazi kapena mamuna wagona ndi munthu amene alinayo
matendayo opanda chitetezo.
- Chindoko chimayamba chifukwa cha tizirombo
tosaoneka ndi maso Zizindikiro zosonyeza kuti muli
ndi chindiko zimatenga masiku angapo, nthawi zina
mpaka masabata angapo kuchokela panthawi yomwe wagona
ndimunthu yemwe ali ndi nthendayo.
-
Dzizindikilo
Amuna amambva kupweteka pokodza. Nthawi zina
mafinya amoeneka kutsogolo kwa chokodzela. Mthawi
zina zizindikiro sizimaoneka konse
- Mwa azimayi nthendayi siyimaoneka ngati mwa
amuna. Azimayi samambva kupweteka kwambiri. Choncho
ndi kwapafupi kuganiza kuti alibe nthendayo. Kamba
kakuti zizindikilo sizimaonekela msanga mwa a zimayi,
nthendayi ndi yowopsya chifukwa amaononga ziwalo
zobelekela mwana.
-
Matendawa ndiochizika mosambvuta ndi
makhwala
HERPES (MASHINGOLS)
- Nthendayi imayamba chifukwa cha tizirombo ta
Virus. Zizindikiro zimachizidwa koma tizirombo
sitimatha mpaka kale kale.
- Zizindikiro zimatenga masiku atatu kufikira
masiku khumi kuchokera patsiku lomwe wagona ndi
munthu amene ali ndi matendawo Zizindikiro
- Matuza amayamba kutuluka, kenaka amayamba
kuphulika and kuuma patapita masiku 5 kufikira 15
- Ngakhale kuti matuzao amapola, tizirombo (virus)
timakhalabe munthupi. Matuza amatulukabe nthawi ndi
nthawi.
- Azimayi sangadziwe kuti ali herpes chifukwa
matuza makhala mkati Mwa amuna matuza matuluka
pachokodzera
MAUKA ( GENITAL WARTS)
- Mauka mayamba chifukwa cha tizirombo (virus)
totchedwa (HUMAN PAPILOMA VIRUS kapena HPV)
- Matuza opanda mafinya amatuluka patapita mwezi
umodzi kufikira chaka chimodzi kuchokera pomwe
nthendayi yatengedwa
- Nthawi ndi nthawi siyimaoneka mwa azimayi,
chifukwa matuzawo amakhala mkati. Mauka ndiopsya mwa
a zimayi chifukwa nthawi zina mayambitsa cancer ya
chibelekelo. Azimayi akulangizidwa kuti adzipimidwa
kawiri kawiri, kuti mwina matenda a cancer
angapezedwe mofulumira asanafalikile kuziwalo zina.
CHIZONONO (SYPHILIS)
- Chizonono chimayamba ndi tizirombo (bacteria)
topatsirana nagti wagona ndi munthu amene ali ndi
matendao. Tizilonda timayamba kuoneka masabata atatu
kufikira miyezi itatu kuchokera panthawi yomwe
watenga matendawo.
- Tizilondati sitimawawa ayi. Patapita milungu
ingapo timapola. Zirombozo (bacteria)zimakhalabe ziri
muthupi. Patapita nthawi tizirindato ti matulukanso
ndi zipere.
- Ziperezo zimathanso patapita nthawi koma
tiziromboto (bacteria) timayamba kuononga ziwaro zina
chizonono chimachizidwa ndi penicillin mosabvuta
- Mwa azimayi tizirondato timabisala mkati.
APHATHA ( PUBIC RICE)
- Aphatha ndi tizirombo tatin'gono kwambiri.
Aphatha amabisala mumabvuzi. Munthu yemwe ali and
aphatha amabva kuyabwa kawirikawiri.
- Tiziromboti timafa ndi makhwala osugunilidwa
mumadzi.
MPHERE (SCABIES)
- Zirombo zoyambitsa mphere ziringati Aphatha.
Kusiyana kwake ndikwakuti zirimbo zopangitsa mphere
zimakhala mkati mwa khungu
- Munthu wa mphere amabva kuyabwa kwambiri. Thupi
lake limadzala ndi tizironda
- Matenda a mphere amachizidwa ndi makhwala a
amadzi popaka mthupi lonse
- Ndikofunika kuchapa zobvala ndi zofunda chifukwa
tiziromboti timabisala muzobvala
VAGINITIS
- Iyi ndi nthenda yomwe imapazeka mwa azimayi.
Mmzimayi yemwe ali ndi nthendayi amakha mafinya
kuchokela mu chibelekelo. Amabva kuthenda pokodza,
mwinanso kununkha.
- Tizirombo tomwe timayambitsa chindoko, chlamydia,
yeast, trichomonas, kapenanso ma bacteria ena
amayambitsa Vaginitis.
- Mafinya amaunikidwa pa microscope pofufuza
nthendayi
- Vaginitis ndiyochizika ngati pali makwala
oyenela.
YEAST INFECTION ( fungus)
- Mafangusi amayambitsa nthendayi
- Mwa Amuna osadulidwa amabva kuyabwa kutsogolo kwa
chokodzera
- Azimayi amakha mafinya oyela ndikuyabwa kwambiri
- Makwala amafangusi amachiza nthendayi mosabvuta
HEPATITIS (MATENDA A CHIWINDI JONDISI)
- Awa ndi matenda oopsya kwambiri omwe amayamba
chifukwa cha ma virus
- Munthu amene ali ndi nthendayi amabva kuzizira
kawiri kawiri, Mmimba mumapweteka kawiri-kawiri,
amakhala otopa nthawi zonse, mkodzo umakhala wa
yellow andi kuda. Maso maoneka chikasu
- Matendawi amantha okha popumula kwambiri.
- Mungathe kudziteteza matendawa polandira katemera
MAGAWA-GAWA (AIDS)
- Awa ndi matenda oopsya kwabiri opatsirana pogona
ndi munthu yemwe ali ndi nthendayi
- Tizirombo ta Magawa-gawa timaononga mbali yathupi
yomwe imateteza kumatenda ena
- Palibe zizindikiro zoonetsa kuti inu kapena akazi
anu muli ndi matendawa pachaka choyamba. Mungadziwe
kuti muli ndi tiziromboti poyezetsa magazi anu
- Munthu wa magawa-gawa amafa patapita zaka
zambiri, mwinanso khumi. Makwala alipo omwe
amachepetsa tizirimboti muthupi lamunthu yemwe ali
ndi matendawa
- Dzitetezeni pobvala mphira ngati mukugona ndi
azimayi kapena azibambo ambiri. Matendawa
amafalitsidwa pobwelekana ma needls and masyringes.
|