CHINDOKO NDI CHLAMYDIA (GONORRHEA NDI CHLAMYDIA)
- Nthenda ya chindoko imayamba pokha pokha ngati mkazi kapena mamuna wagona ndi munthu amene alinayo matendayo opanda chitetezo.
- Chindoko chimayamba chifukwa cha tizirombo tosaoneka ndi maso Zizindikiro zosonyeza kuti muli ndi chindiko zimatenga masiku angapo, nthawi zina mpaka masabata angapo kuchokela panthawi yomwe wagona ndimunthu yemwe ali ndi nthendayo.
- Dzizindikilo
Amuna amambva kupweteka pokodza. Nthawi zina mafinya amoeneka kutsogolo kwa chokodzela. Mthawi zina zizindikiro sizimaoneka konse
- Mwa azimayi nthendayi siyimaoneka ngati mwa amuna. Azimayi samambva kupweteka kwambiri. Choncho ndi kwapafupi kuganiza kuti alibe nthendayo. Kamba kakuti zizindikilo sizimaonekela msanga mwa a zimayi, nthendayi ndi yowopsya chifukwa amaononga ziwalo zobelekela mwana.
- Matendawa ndiochizika mosambvuta ndi makhwala
HERPES (MASHINGOLS)
- Nthendayi imayamba chifukwa cha tizirombo ta Virus. Zizindikiro zimachizidwa koma tizirombo sitimatha mpaka kale kale.
- Zizindikiro zimatenga masiku atatu kufikira masiku khumi kuchokera patsiku lomwe wagona ndi munthu amene ali ndi matendawo
Zizindikiro
- Matuza amayamba kutuluka, kenaka amayamba kuphulika and kuuma patapita masiku 5 kufikira 15
- Ngakhale kuti matuzao amapola, tizirombo (virus) timakhalabe munthupi. Matuza amatulukabe nthawi ndi nthawi.
- Azimayi sangadziwe kuti ali herpes chifukwa matuza makhala mkati Mwa amuna matuza matuluka pachokodzera
MAUKA ( GENITAL WARTS)
- Mauka mayamba chifukwa cha tizirombo (virus) totchedwa (HUMAN PAPILOMA VIRUS kapena HPV)
- Matuza opanda mafinya amatuluka patapita mwezi umodzi kufikira chaka chimodzi kuchokera pomwe nthendayi yatengedwa
- Nthawi ndi nthawi siyimaoneka mwa azimayi, chifukwa matuzawo amakhala mkati. Mauka ndiopsya mwa a zimayi chifukwa nthawi zina mayambitsa cancer ya chibelekelo. Azimayi akulangizidwa kuti adzipimidwa kawiri kawiri, kuti mwina matenda a cancer angapezedwe mofulumira asanafalikile kuziwalo zina.
CHIZONONO (SYPHILIS)
- Chizonono chimayamba ndi tizirombo (bacteria) topatsirana nagti wagona ndi munthu amene ali ndi matendao. Tizilonda timayamba kuoneka masabata atatu kufikira miyezi itatu kuchokera panthawi yomwe watenga matendawo.
- Tizilondati sitimawawa ayi. Patapita milungu ingapo timapola. Zirombozo (bacteria)zimakhalabe ziri muthupi. Patapita nthawi tizirindato ti matulukanso ndi zipere.
- Ziperezo zimathanso patapita nthawi koma tiziromboto (bacteria) timayamba kuononga ziwaro zina
chizonono chimachizidwa ndi penicillin mosabvuta
- Mwa azimayi tizirondato timabisala mkati.
APHATHA ( PUBIC RICE)
- Aphatha ndi tizirombo tatin'gono kwambiri. Aphatha amabisala mumabvuzi. Munthu yemwe ali and aphatha amabva kuyabwa kawirikawiri.
- Tiziromboti timafa ndi makhwala osugunilidwa mumadzi.
MPHERE (SCABIES)
- Zirombo zoyambitsa mphere ziringati Aphatha. Kusiyana kwake ndikwakuti zirimbo zopangitsa mphere zimakhala mkati mwa khungu
- Munthu wa mphere amabva kuyabwa kwambiri. Thupi lake limadzala ndi tizironda
- Matenda a mphere amachizidwa ndi makhwala a amadzi popaka mthupi lonse
- Ndikofunika kuchapa zobvala ndi zofunda chifukwa tiziromboti timabisala muzobvala
VAGINITIS
- Iyi ndi nthenda yomwe imapazeka mwa azimayi. Mmzimayi yemwe ali ndi nthendayi amakha mafinya kuchokela mu chibelekelo. Amabva kuthenda pokodza, mwinanso kununkha.
- Tizirombo tomwe timayambitsa chindoko, chlamydia, yeast, trichomonas, kapenanso ma bacteria ena amayambitsa Vaginitis.
- Mafinya amaunikidwa pa microscope pofufuza nthendayi
- Vaginitis ndiyochizika ngati pali makwala oyenela.
YEAST INFECTION ( fungus)
- Mafangusi amayambitsa nthendayi
- Mwa Amuna osadulidwa amabva kuyabwa kutsogolo kwa chokodzera
- Azimayi amakha mafinya oyela ndikuyabwa kwambiri
- Makwala amafangusi amachiza nthendayi mosabvuta
HEPATITIS (MATENDA A CHIWINDI JONDISI)
- Awa ndi matenda oopsya kwambiri omwe amayamba chifukwa cha ma virus
- Munthu amene ali ndi nthendayi amabva kuzizira kawiri kawiri, Mmimba mumapweteka kawiri-kawiri, amakhala otopa nthawi zonse, mkodzo umakhala wa yellow andi kuda. Maso maoneka chikasu
- Matendawi amantha okha popumula kwambiri.
- Mungathe kudziteteza matendawa polandira katemera
MAGAWA-GAWA (AIDS)
- Awa ndi matenda oopsya kwabiri opatsirana pogona ndi munthu yemwe ali ndi nthendayi
- Tizirombo ta Magawa-gawa timaononga mbali yathupi yomwe imateteza kumatenda ena
- Palibe zizindikiro zoonetsa kuti inu kapena akazi anu muli ndi matendawa pachaka choyamba. Mungadziwe kuti muli ndi tiziromboti poyezetsa magazi anu
- Munthu wa magawa-gawa amafa patapita zaka zambiri, mwinanso khumi. Makwala alipo omwe amachepetsa tizirimboti muthupi lamunthu yemwe ali ndi matendawa
- Dzitetezeni pobvala mphira ngati mukugona ndi azimayi kapena azibambo ambiri. Matendawa amafalitsidwa pobwelekana ma needls and masyringes.
|